Ndondomeko Zosakakamiza Zolimbikitsa Ntchito Zing’onozing’ono Za Usodzi Zokhalitsa
No hay miniatura disponible
Fecha
Autores
Título de la revista
ISSN de la revista
Título del volumen
Editor
FAO ;
Resumen
Descripción
Ndondomeko zolimbikitsa usodzi oyenera kwa asodzi an’gonoan’gono ndi zimene zikulondoloza m’mene usodzi ungamachitikire m’maiko onse. Ndondomekoyi inakhazikitsidwa m’chaka cha 2011 itavomerezedwa ndi komiti yoyang’anira usodzi pa dziko lonse, yotchedwa Committee on Fisheries (COFI) m’chingerezi. Ndondomekoyi ili ndi zolinga zofanana ndi ndondomeko zina monga za m’mene kaphedwe ka nsomba kakuyenera kumachitikira m’nyanja ndi m’mitsinje (code of conduct for responsible fisheries), kuganizira maufulu a anthu pakapezedwe kachakudya (VG Tenure and the Right to Food Guidelines). Ndondomekozi zatsamira pa danga loti asodzi azitha kumapha nsomba zokwanira kuti athe kumadya zina nkumagulitsa, motero nkumachepetsa umphawi pakati pawo. Ndondomekoyi inakhazikitsidwa ndi kuvomerezedwa ndi maiko onse atakambirana ndi adindo a mabungwe okhudzidwa ndi za usodzi okwana 4 000 motsogozedwa ndi bungwe la FAO litapatsidwa mphamvu ndi komiti yaza usodzi ya COFI. Maiko, magulu a zausodzi komanso mabungwe ena onse akupemphedwa kutengapo gawo powonetsetsa kuti asodzi, maka asodzi an’gono an’gono, anthu ogwira ntchito za usodzi ndi ena onse akupindula potsata ndondomekoyi. Tikutsindika kuti anthu amene ali ovutikitsitsa (maka amayi, ana, olumala ndi ena otero) ayenera kutenga nawo mbali pokhazikitsa ziganizo ndi mfundo zakayendetsedwe ka ntchito za usodzi m’madera mwawo.
